. Changamire M’zizi (Kantini Samson) is a Zambian poet, a development educationalist, and a cultural historian. He is interested in the aims, the strategies, and the content of the socialization and transformative processes that they ought to have in place to create, promote and raise the critical consciousness of wholeness in low-resourced environments in order to bridge the divide between the worlds of rich and poor, and the theory and practice for sustainable societies. He holds a Ph.D. in Education from Seoul National University, an MEd in Education and Development from The University of Zambia (UNZA), an MA in Literature, and a BA in Education (BAEd) also from UNZA. He has received a Certificate in Diplomatic Practice, Protocol, and Public Relations from the Zambia Institute of Diplomacy and International Studies (ZIDIS). Currently, He is Senior Programme Officer for Culture, Communication and Information at the Zambia National Commission for the United Nations Educational, Scientific and Cultural Organisation (UNESCO)

냔자어/체와어(Nyanja/Chewa) : 체와어(Chewa)는 말라위의 공용어이다. 니제르콩고어족에 속하며 냔자어(Nanja)로도 알려져 있다. 시인은 모어(母語)인 냔자어(Nyanja)/체와어(Chewa)로 이야기의 내용, 그 속의 인물들, 그것이 지니는 문화적 가치 등의 이미지와 격언과 비유를 표현한다.

 

N’cifukwa ciani
Malisece, cinthako mulowa, mungena mumpako ya njuchi?
Zizakulumani
Kunzuna kwa uchi nimfiti yamalaza (yakanthu)!

N’cifukwa nciani
Citseko'co sicotseka?
Onani njoka yotawa mpepo ya Juni (mwina Julai mpepo)
Izakulumani inu njoka'yi ikafunda; italowamo!

Nthawi zina njoka ibisama mumpako ya njuchi,
Kudyako tiana tikumela mapepe kumwelapo na uchi
Inu ofula mufuleko, icho chusi sichisewenza.
Tengani zobvala mubveke thupi kumodzi na muthu.

Bvalani-bvalani
Imwe njuchi izi ziluma zedi (zipaya)
Piringupiringu ngwa njuchi, yoluma ndi imodzi

Bvalani-bvalani
Imwe njoka'yi ilibe mankhwala
Kalikwikwiti saluma, koma akaluma alibe chivumulo!

Bvalani-bvalani
Imwe njoka'yi, mitu ziwiri (niyamaloza)
Kumutu kwako tsitsi
Kukuti sunga bongo-bongo wako
Nzeru yakuya ngati Chiswe (Muswa)

Pamaso pako nsiye
Pakuti sunga maso ako
Cimaso-maso, golidi sizonse zing’anima

Mumakhutu ako ubweya
Akuti sunga makhutu ako
Umoyo wa munthu uli m’khutu
Samva zaanzake anamva nkwangwa ili m’muthu

M'mpuno mwako ubweya
Mukuti sunga mpuno zako
Nunsha-nunsha adanunsha ndi tuvi

Pamulomo pako ndebvu
Pakuti ndani angazoloweretse lilime?
Mpamvu ya imfa ndi moyo zili palilime
Zakudya ndi zakumwa usamalile
Maidya-idya amakono ndi imfa

Kukalevu-levu kako ndebvu!
Kakuti sunga mukosi wako
Ulungu ndi umulungu umapezeka

Munkhwapata mwako tsitsi
Mukuti bisa mtima wako
Dziko lino liri ndi mano

Pachinena pako mavuzi
Pakuti lemekeza cobisika'co;
Ndiye lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano.
Ngodala okesa mwazi wacinamwali pakama laukwati;
Alibe ziwanda zogwebana ndi okondedwa ace

Panthaka mauzu ndi mitengo
Pakunena sunga zamdothi, mmadzi ndi mlenge-mlenga
Chuma chili mnthaka
Atsamunda asakubere cuma cacikalire

Tsopano taona timaziba tako twakula tuliciliri
Tukunena munthu wanga'we limba ngati mliri
Anyamata azibambo asakupwanye-pwanye

Timahipu nato tafufumuka
Tikunena, thupi langa'we osafoka
Anyamata, azibambo asakushotokole.

Kachiuno kako kayamba kupita kumwezi
Kakuti iwe tsono ndiwe nyenyezi
Maso onse amu m’dima ali tsono pa iwe
Kulowa kwadzuwa iwe nyenyezi,
Kusakupeza kunja kwanyumba yamako.

Samalila cinamwali cisungu cako ngati dzira
Dzira siliola tsiku limodzi
Chizolowezi ca kholowa chinadyetsa mbatata pansi
Unamwali wako ndiwo moyo wako

Mnyamata nawe penya tsopano
Tumapolo twako twapombosoka,
Tukunena kuti munthu wanga'we longosoka.
Atsikana, azimai asakupange Shepolopolo bola

Kavoice kako kakhala dipi
Kakamba ati thupi lako ndilam'tengo wapatali.
Cikomekome cankhuyu nimfiti
Atsikana azimai azakuikisa 6-6-6 fiti.

Tumamaso twako twapangika molimba,
Tukuti bvina Nyau Makishi upewe tsoka
Maboza ukupukhawo Satana njoka
Ucamuna ndi kutukula moyo wako ndi dziko

Bvalani-bvalani
Imwe njuchi izi ziluma zedi (zipaya)
Piringupiringu ngwa njuchi, yoluma ndi imodzi
Kalikwikwiti saluma, koma akaluma alibe chivumulo!
 

저작권자 © 더스쿠프 무단전재 및 재배포 금지

개의 댓글

0 / 400
댓글 정렬
BEST댓글
BEST 댓글 답글과 추천수를 합산하여 자동으로 노출됩니다.
댓글삭제
삭제한 댓글은 다시 복구할 수 없습니다.
그래도 삭제하시겠습니까?
댓글수정
댓글 수정은 작성 후 1분내에만 가능합니다.
/ 400

내 댓글 모음